ZAMPIRA
MWANA NDI MWANA : FINALI KUTCHAYA KUGWESA Associates: osewera mpira ndi Phuzitsi wa mkulu T imu ya osewera ya mpira wa miyendo omwe ndi ma associate, inapambana zigoli ziwiri kwa chimodzi , loweruka lapitali pa bwalo la zamasewero la agriculture.Masewera omwe anali pakati pa ma associate omwe ndi ophuzira a m’mchaka chachitatu , ndi ophuzira a m’mchaka chomaliza( year 4) . Ma associate ndiwo amastogola chigawo choyamba pomwe anapeza chigoli kudzera mwa Penjan chunga osewera pa nambala 7 ndipo pa mphindi khumi , ma finali anapeza chigoli kudzera mwa Mbekeyani zomwe zinapangisa mbali zose ziwiri kufanana zigoli mu chigawo choyamba . Ngankhale izi zili chomchi , ma associate anakwanisa kuonjezera mphavu pamene anapeza chigoli china mu mphindi 75 kudzera mwa Zax chomwe anaperekera ndi Phade osewera kutsogolo pa nambala 9. Poyakhula ndi Twinkle Alex Mtonda, yemwe anati ndi Phuzitsi wawo wa mkulu ,anati masewera anali bwino kwambiri ndipo osewera ake anac...