ZAMPIRA

 MWANA NDI MWANA : FINALI KUTCHAYA KUGWESA 

Associates: osewera mpira ndi Phuzitsi wa mkulu 

 Timu ya osewera ya mpira wa miyendo omwe ndi ma associate, inapambana zigoli ziwiri kwa chimodzi , loweruka lapitali pa bwalo la zamasewero la agriculture.Masewera omwe anali pakati pa ma associate omwe ndi ophuzira a m’mchaka chachitatu , ndi ophuzira a m’mchaka chomaliza( year 4) .

Ma associate ndiwo amastogola chigawo choyamba pomwe anapeza chigoli kudzera mwa Penjan chunga osewera pa nambala 7 ndipo pa mphindi khumi , ma finali anapeza chigoli kudzera mwa Mbekeyani  zomwe zinapangisa mbali zose ziwiri kufanana zigoli mu chigawo choyamba .

Ngankhale izi zili chomchi , ma associate anakwanisa kuonjezera mphavu pamene anapeza chigoli china mu mphindi 75 kudzera mwa Zax chomwe anaperekera ndi Phade osewera kutsogolo pa nambala 9.

Poyakhula ndi Twinkle Alex Mtonda, yemwe anati ndi Phuzitsi wawo wa mkulu ,anati masewera anali bwino kwambiri ndipo osewera ake anachita bwino pomwe amapita pita kustogolo kusiyana ndi ma finali.

" Latsoka ndi latsoka , mtengo umatelera ndithu olo nyani ayesele kukwera amakanika , kukana chigoli chomwe oyimbira anachovomereza sikunawapindulire ", Mtonda anafotokoza 

Poyikirapo ndemanga za kukanidwa chigoli , A Mtonda anati ,Kutengera ndi mbiri ya ma finali chiyambireni masewera ma sabata apitawa ,game yawo yoyamba ndi ma year 1 komaso yachiwiri ndi ma konti sinathe bwino amagwirisa ntchito offside trap kufuna kubera chipambano chawo .

Izi zikutathauza kuti ma associate ndiamene ali  akastwiri a principal's Trophy 2024 kaning'ina campus,pamene amaliza ndi ma points 7 ,zigoli ziwiri masewero a miyendo .


Olemba ,

 ALINAFE JONAS 

Comments

Post a Comment

Popular posts from this blog

ARTS

Entertainment

Politics